“The best time to plant a tree was 20 years ago. The second-best time is now.” (Chinese Proverb)

Mwina mumawona ngati ena anabadwa ndi mwayi wapadera kapena ndalama zinangowanja kwa iwo, koma chowonadi n’chakuti aliyense ali ndi mwayi woti akhale wopambana. M’moyo, zomwe tili nazo zimatengera kwambiri mmene timagwiritsira ntchito zomwe tili nazo. Ngakhale titachokera kumabanja a umphawi, nafe tili ndi mwayi woti tisinthe moyo wathu ngati tikhazikika pa khama ndi luso.

Ndikufuna ndigawane nazu nkhani za chuma ndi njira zokwaniritsira zolinga zanu, makamaka kwa ife achinyamata. Nthawi zambiri, timataya nthawi ndi ndalama pazinthu zopanda phindu pamene ndifenso oshota ndikale. Masiku ano, kulibe chifukwa cholola kukhala mbuli chifukwa mwayi wophunzira uli pafupi nafe zedi kudzera pa internet.

Phindu la Intaneti ndi Maphunziro Aulere

Pa YouTube, pali maphunziro osiyanasiyana a chilichonse chomwe mungafune kuphunzira—chiyankhulo chatsopano, luso lina, zokhuza mbiri, kapena zachuma. Komabe, anthu ambiri timasankha kutaya nthawi yathu kuchedza pa TikTok, Instagram, Facebook, ndi WhatsApp. Ndi zomvetsa chisoni kuti timakhala ndi nthawi yokwanira pa masamba a nchezo koma sitipeza nthawi yophunzira kapena kugwira ntchito zina zofunikira.


Mwachitsanzo:
M’malo mopereka ndalama zanu zonse ku data yochezera pa masamba amchezo, mugwiritse ntchito ma bandulo omwewo kuphunzira luso latsopano kapena kuchita kafukufuku.

Mu 2025, kodi mukufuna kuchita chiyani? Tangoganizani izi:

  1. Kuyamba Kusunga Ndalama:
    Ndalama zomwe mumagwiritsa ntchito pa bandulo yochedzera pa intaneti, mukhoza kuzigwiritsa ntchito kugula ma shares ku Malawi Stock Exchange.
    Mwachitsanzo, ma shares a TNM lero akugulitsidwa pa K20. Ndi K5,000 mukhoza kugula ma shares 250. Mu miyezi inayi, mukakhala ndi ma shares 1,000!
  2. Kuphunzira Luso Latsopano:
    Mwachitsanzo, mukufuna kuphunzira kuyimba guitar kapena piano, koma mulibe ndalama zokwanira zopereka kwa mphunzisi oti akuphunzitseni kuyimbako, Osadandaula! Maphunziro aulere alipo pa YouTube. Ngati mungayambe kuphunzira lero, ndi khama, pofika May, mudzakhala okonzeka kuyesera kuyimba kugulu.

Tangoyambanipo

Simudzapeza nthawi yokwanira yoti mukwaniritse zolinga zanu ngati simungapatulire nthawi yochita zomwezo. Zomwe mungayambe kuchita lero, musadikire kuti zinthu zikhale pabwino (Don’t wait for the perfect opportunity because it will never come).

Pedzani bokosi losungira ndalama: Mudzisunga pang’ono tsiku lililonse kuchokera kuphindu mukupanga pa malonda anu kapena ndalama zina. Mukhoza kuyambapo kusunga Mk1,000 kapena Mk2,000 tsiku lililonse. Pomaliza, muwone ndalama zomwe mwasonkhanitsa kumapeto kwa mlungu. Mutha kudziika ku banki kapena kugulira ma shares.

Mukangoyambapo, mphamvu yopitiriza idzabwera yokha. Pedzani mnzanu amene angakulimbikitseni kuti musinthe moyo wanu. Musanazindikire, mudzakhala mwayamba ulendo wopita ku chuma komanso tsogolo labwino.

Kodi mukufuna chiyani mu 2025? Tangoyambanipo basi.

“An investment in Knowledge pays the best interest.” (Benjamin Franklin)

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Share this post

Subscribe to our newsletter

Keep up with the latest blog posts by staying updated. No spamming: we promise.
By clicking Sign Up you’re confirming that you agree with our Terms and Conditions.

Related posts